Acts 21:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mkulu wa asilikali uja adafika nagwira Paulo, nkulamula kuti ammange ndi maunyolo aŵiri. Kenaka adafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndani? Ndipo watani kodi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa asilikaliyo anabwera nagwira Paulo, ndipo analamula kuti amangidwe ndi maunyolo awiri. Kenaka iye anafunsa kuti ndi ndani ndipo wachita chiyani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?