Acts 21:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pakati pa anthuwo ena adayamba kufuula zina, ena zina. Chifukwa cha phokosolo mkulu wa asilikali uja sadathe kudziŵa kuti zoona zenizeni nziti. Choncho adalamula kuti amtenge Pauloyo apite naye ku linga la asilikali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wina anafuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.