Acts 21:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali pafupi kuloŵa naye m'lingamo, Paulo adapempha mkulu wa asilikali uja kuti, “Kodi mungandilole kuti ndikuuzeni kanthu?” Iye adati, “Kani umalankhula Chigriki?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asilikali ali pafupi kulowa naye ku malo awo, iye anapempha mkulu wa asilikaliyo kuti, “Kodi mungandilole ndiyankhulepo?” Mkulu wa asilikaliyo anafunsa kuti, “Kodi umayankhula Chigriki?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkuru, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Cihelene?