Acts 21:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndiye kuti sindiwe Mwejipito uja udautsa chipolowe masiku apitawo nkutsogolera zigaŵenga zikwi zinai kupita nazo ku chipululu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi sindiwe Mwigupto uja amene masiku apitawo unayambitsa kuwukira ndi kutsogolera anthu 4,000 owukira aja nʼkupita nawo ku chipululu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si ndiwe M-aigupto uja kodi, unacita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kucipululu?