Acts 21:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paulo adayankha kuti, “Inetu ndine Myuda, nzika ya ku Tariso, mzinda wotchuka wa ku Silisiya. Ndikukupemphani tsono, mundilole kuti ndilankhule nawo anthuŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Silisiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo anayankha kuti, “Ine ndine Myuda, wa ku Tarisisi ku Kilikiya. Sindine nzika ya mzinda wamba. Chonde loleni ndiyankhule nawo anthuwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Kilikiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.