Acts 21:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamloladi, ndipo Paulo adaima pamakwerero paja, naweyula dzanja kuti anthuwo akhale chete. Pamene onse adakhala chete, Paulo adayamba kulankhula nawo pa Chiyuda. Adati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ataloledwa ndi mkulu wa asilikaliyo, Paulo anayimirira pa makwereropo nakweza dzanja lake kwa gulu la anthuwo. Onse atakhala chete, iye anayankhula nawo mʼChihebri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala cete onse, analankhula nao m'cinenedwe ca Cihebri, nanena.