Acts 21:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene masiku athu aja adatha, tidachokako nkupitirira ulendo wathu. Onsewo, pamodzi ndi akazi ao ndi ana awo omwe, adatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Tidagwada pa mchenga m'mbali mwa njanja nkupemphera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nthawi yathu itatha, tinachokako ndi kupitiriza ulendo wathu. Ophunzira onse pamodzi ndi akazi awo ndi ana anatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Ndipo kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja ndi kupemphera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidacoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana anatiperekeza kufikira kuturuka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mcenga wa kunyanja, tinapemphera,