Acts 21:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake tidanyamuka nkukafika ku Kesareya. Tidapita kunyumba kwa mlaliki Filipo, mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri aja, ndipo tidakhala kunyumba kwakeko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace tinacoka, ntinafika ku Kaisareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.