Acts 22:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adandiwuza kuti, ‘Mulungu wa makolo athu adakusankha kuti udziŵe zimene Iye akufuna, uwone Wolungama uja, ndipo umve mau ake olankhula nawe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe cifuniro cace, nuone Wolungamayo, numve mau oturuka m'kamwa mwace.