Acts 22:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira, tuluka msangamsanga m'Yerusalemu muno, chifukwa anthuŵa sadzauvomera umboni wako wonena za Ine.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinamuona iye, nanena nane, Fulumira, turuka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.