Acts 22:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo mkulu wa asilikali uja adalamula kuti aloŵe naye Paulo m'linga la asilikali lija. Adaŵauza kuti amkwapule, kuti iyeyo aulule chifukwa chimene anthu aja ankamukuwizira chotere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapitao wamkuru analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe cifukwa cace nciani kuti ampfuulira comweco.