Acts 22:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkulu uja adamuuza kuti, “Ine ndidachita chogula ufulu wangawu ndi ndalama zambiri.” Paulo adati, “Koma ine wangawu ndidachita chobadwa nawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.” Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kapitao wamkuru anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wace waukuru. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.