Acts 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inetu ndiye Myuda mbadwa ya ku Tariso, mzinda wa ku Silisiya, koma ndidaleredwa mu mzinda wa Yerusalemu mom'muno. Gamaliele ndiye anali mphunzitsi wanga amene adandiphunzitsa kwenikweni kusunga Malamulo a makolo athu. Ndipo ndinkalimbikira kwambiri pa za Mulungu, monga momwe mukuchitira nonsenu lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Kilikiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliyeli, wolangizidwa monga mwa citsatidwe ceni ceni ca cilamulo ca makolo athu, ndipo ndinali wacangu, colinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;