Acts 22:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa asilikali uja adaafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adaadzanenezera Paulo. Choncho m'maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse a pa Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mawa mwace pofuna kuzindikira cifukwa cace ceni ceni cakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe akulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.