Acts 22:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa ansembe onse ndi onse a m'Bungwe la akuluakulu a Ayuda angathe kundivomereza. Iwowo adaandipatsa makalata opita nawo kwa abale athu achiyuda ku Damasiko. Tsono ndidapita komweko kuti ndikaŵagwire anthu ameneŵa, ndi kubwera nawo ku Yerusalemu ali omangidwa, kuti adzalangidwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monganso mkulu wa ansembe andicitira umboni, ndi bwalo lonse la akuru; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.