Acts 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adafika pokangana koopsa, kotero kuti mkulu wa asilikali uja ankaopa kuti angamkadzule Paulo. Choncho adalamula asilikali kuti, “Pitani mukamlanditse kwa anthuwo, mukamloŵetse m'linga la asilikali.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkangano unakula kwambiri kotero kuti mkulu wa asilikali anachita mantha kuti mwina anthu angakhadzule Paulo. Iye analamulira asilikali ake apite kukamuchotsa pakati pawo mwamphamvu ndi kubwera naye ku malo a asilikaliwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene padauka cipolowe cacikuru, kapitao wamkuru anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikari atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga,