Acts 23:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adamtengadi mnyamatayo kupita naye kwa mkulu wa asilikali, namuuza kuti, “Mkaidi uja Paulo anandiitana, nandipempha kuti ndibwere ndi mnyamatayu kwa inu, akuti ali nanu ndi mau.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkuru, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.