Acts 23:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa asilikali uja adamgwira pa dzanja mnyamatayo, namtengera pambali, ndipo ali paokha adamufunsa kuti, “Kodi ndi mau anji ukufuna kundiwuza?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa asilikali uja anagwira dzanja mnyamatayo napita naye paseli ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti undiwuze chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kapitao wamkuru anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Ciani ici uli naco kundifotokozera?