Acts 23:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adati, “Ayuda ena apangana zodzakupemphani kuti mupite ndi Paulo ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu maŵa, ngati kuti iwowo akufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa ku bwalo la mirandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.