Acts 23:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pepani, inu musaŵamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anai amene akukamlalira Paulo pa njira. Iwowo alumbira kuti sadzadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha. Panopa ali okonzeka ndipo akungodikira kuti inu muŵabvomere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu musawamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anayi amene akumudikirira pa njira. Iwo alumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Panopa ndi okonzeka kale, akungodikira kuti muwavomere pempho lawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kud sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.