Acts 23:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo Ayuda adaamugwira, ndipo anali pafupi kumupha. Nditamva kuti iyeyo ndi mfulu wachiroma, ndidapita ndi asilikali nkukamlanditsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo Ayuda anamugwira ndipo anali pafupi kumupha, koma ine ndinapita ndi asilikali nʼkukamulanditsa pakuti ndinamva kuti ndi nzika ya Chiroma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikari, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.