Acts 23:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti ndamva kuti pali chiwembu chimene ampanganirana munthuyu, ndamtumiza kwa inu msanga. Ndauza omnenezawo kuti adzanene mau ao kwa inu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditawuzidwa kuti amukonzera chiwembu munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga. Ine ndalamulanso amene akumuyimba mlanduwo kuti abwere kwa inu kudzafotokoza nkhaniyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali ciwembu ca pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.