Acts 23:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Paulo adaona kuti ena mwa iwo ndi a m'gulu la Asaduki, ena a m'gulu la Afarisi, adanena mokweza mau m'Bwalo muja kuti, “Abale anga, inetu ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ineyo ndikuweruzidwa chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu adzauka kwa akufa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo atazindikira kuti ena mwa iwo anali Asaduki ndiponso ena anali Afarisi, anafuwula mʼbwalo muja kuti, “Abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anapfuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa ciyembekezo ndi kuuka kwa akufa.