Acts 23:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adayamba kufuula kwambiri. Tsono aphunzitsi ena a Malamulo, a m'gulu la Afarisi, adaimirira nanenetsa kuti, “Sitikupeza konse cholakwa mwa munthuyu ai. Mwina nkukhala kuti mzimu kapena mngelo walankhula naye!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali phokoso lalikulu, ndipo aphunzitsi ena amalamulo amene anali a gulu la Afarisi anayimirira natsutsa kwambiri. Iwo anati, “Ife sitikupeza cholakwa ndi munthu uyu, chifukwa mwina ndi mzimu kapena mngelo amene wayankhula naye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cidauka cipolowe cacikuru; ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza coipa ciri conse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo: walankhula naye?