Acts 24:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita masiku asanu, Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adadza pamodzi ndi akuluakulu ena a Ayuda, ndi katswiri wina wolankhulira anthu pa milandu, dzina lake Tertulo. Iwo adafika pamaso pa bwanamkubwa uja, nayamba kuneneza Paulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita masiku asanu mkulu wa ansembe Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena ndi katswiri woyankhulira anthu pa milandu wotchedwa Tertuliyo anapita ku Kaisareya ndipo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa Bwanamkubwayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Hananiya pamodzi ndi akuru ena, ndi wogwira moyo dzina lace Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.