Acts 24:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwanamkubwa uja adakodola Paulo kuti alankhule, ndipo Paulo adati, “Ndikudziŵa kuti inu mwakhala mukuweruza mtundu uwu zaka zambiri tsopano, nchifukwa chake ndakondwa kuti ndiyankhe pamaso panu zimene akundinenezazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bwanamkubwayo atakodola Paulo ndi kulola kuti ayankhule, Pauloyo anati, “Ine ndikudziwa kuti inu mwakhala mukuweruza dziko lino zaka zambiri, kotero ndikukondwera kuti ndikudziteteza ndekha pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;