Acts 24:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ichi chokha ndikuvomera pamaso panu, kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu potsata Njira imene iwoŵa amati ndi gulu lopatulika. Ndimakhulupirira zonse zolembedwa m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu ine ndikuvomera kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu, monga wotsatira wa Njirayo, imene iwo akuyitchula mpatuko. Ine ndimakhulupirira chilichonse chimene chimagwirizana ndi malamulo ndiponso zimene zinalembedwa ndi Aneneri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ici ndibvomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupira zonse ziri monga mwa cilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;