Acts 24:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Pauloyo atamuitana, Tertulo uja adayambapo zomunenezazo. Adati, “Inu a Felikisi olemekezeka, ife tikukhala pa mtendere weniweni chifukwa cha inu, ndipo zinthu zambiri zakhala zikukonzeka m'dziko mwathu chifukwa cha utsogoleri wanu wanzeru.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamuyitana Paulo, ndipo Tertuliyo anafotokozera Felike nkhani yonse ya Paulo. Iye anati, “Wolemekezeka, ife takhala pamtendere nthawi yayitali chifukwa cha inu, ndipo utsogoleri wanu wanzeru wabweretsa kusintha mʼdziko lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena. Popeza tiri nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,