Acts 24:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Felikisi ankadziŵa bwino za Njira ya Ambuye, choncho adatseka bwalolo ndi mau akuti, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera Lisiasi, mkulu wa asilikali.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Felike, amene amadziwa bwino za Njirayo, anayamba wayimitsa mlanduwo, nati, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera mkulu wa asilikali Lusiya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Felike anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lusiya kapitao wamkuru akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.