Acts 24:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene Paulo adakamba za chilungamo, za kudziletsa, ndi zakuti Mulungu adzaweruza anthu, Felikisi adachita mantha namuuza kuti, “Pakali pano bapita, ndikapeza nthaŵi, ndichita kukuitananso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo atayankhula za chilungamo, za kudziretsa ndiponso za chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha ndipo anati, “Basi tsopano! Pita. Tidzakuyitanitsa tikadzapeza mpata.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene anamfotokozera za cilungamo, ndi cidziletso, ndi ciweruziro cirinkudza, Felike anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.