Acts 24:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ankaganiza kuti Paulo adzampatsa ndalama, nchifukwa chake ankamuitana kaŵirikaŵiri namacheza naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyi amayembekeza kuti Paulo adzamupatsa ndalama, nʼchifukwa chake amamuyitanitsa kawirikawiri ndi kumayankhula naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; cifukwa cacenso anamuitana iye kawiri kawiri, nakamba naye.