Acts 25:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Paulo adati, “Ine ndaima pa bwalo lamilandu la Mfumu ya ku Roma, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ayudaŵa ine sindidaŵalakwire chilichonse, monga inu mukudziŵa bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitira kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo anayankha kuti, “Ine tsopano ndayima pamaso pa bwalo la milandu la Kaisara, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ine sindinalakwire Ayuda, monga inu mukudziwa bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Paulo anati, ndirikuimirira pa mpando waciweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawacitira-kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.