Acts 25:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati ndili wolakwa, ndipo ngati ndachita kanthu koyenera kuti ndiphedwe, sindikukana kuphedwa ai. Koma ngati zimene aŵa akundinenezazi si zoona, palibe munthu angathe kundipereka kwa iwo. Ine ndikupempha kuti mlandu wangawu ndikagwade kwa Mfumu ya ku Roma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati ndili wolakwa, ngati ndachita kanthu koyenera kuphedwa, ine sindikukana kufa. Koma ngati mlandu umene abweretsa Ayudawa siwoona, palibe munthu angathe kundipereka mʼmanja mwawo. Ndikupempha kuti ndikaweruzidwe ndi Kaisara!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ngati ndiri wocita zoipa, ngati ndacita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zacabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditurukira kwa Kaisara.