Acts 25:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Fesito atakambirana ndi abwalo ake, adati, “Wachita apilo kwa Mfumu ya ku Roma. Chabwino, udzapitadi ku Romako kwa Mfumu yaikulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Fesito, atakamba ndi aphungu ake, anayankha, Wanena, Nditulukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Festo atakambirana ndi akuluakulu abwalo lake, anati, “Popeza wapempha kupita kwa Kaisara, kwa Kaisara udzapitadi!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Festo, atakamba ndi aphungu ace, anayankha, Wanena, Ndirurukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.