Acts 25:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ndinali ku Yerusalemu, akulu a ansembe pamodzi ndi atsogoleri a Ayuda adandifotokozera za iye, nandipempha kuti ndizenge mlandu wake ndi kugamula kuti ngwolakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndili ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditapita ku Yerusalemu akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda anandifotokozera mlandu wake ndipo anandipempha kuti ndigamule kuti ndi wolakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene ansembe akulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wace.