Acts 25:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidaŵayankha kuti si mwambo wa Aroma kungompereka munthu ai. Munthu wonenezedwayo amayamba wakumana nawo omnenezawo, kuti iyeyo akhale ndi mwai woyankhapo pa zimene akumnenezazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndinawayankha kuti si mwambo wa Aroma kungomupereka munthu ayi. Munthu woyimbidwa mlanduyo amayenera kukumana nawo omunenezawo, kuti iye akhale ndi mwayi woyankhapo pa zimene akumuyimba mlanduzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinawayankha, kuti macitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa comneneraco.