Acts 25:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwo atadzasonkhana kuno, ineyo mosataya nthaŵi, m'maŵa mwake ndidakakhala pa mpando woweruzira milandu, nkumuitanitsa munthuyo kuti abwere pamaso panga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero, pamene adasonkhana pano, sindinachedwa, koma m'mawa mwake ndinakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atabwera kuno pamodzi ndi ine, sindinachedwetse mlanduwo, koma ndinayitanitsa bwalo mmawa mwake ndi kulamula kuti amubweretse munthuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero, pamene adasonkhana pano, sindinacedwa, koma m'mawa mwace ndinakhala pa mpando waciweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.