Acts 25:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere mfumuyo za iyeyu. Motero ndabwera naye kwa inu, makamaka kwa inuinuyo mfumu Agripa, kuti mutamufunsitsa, ndikhale nkanthu koti ndilembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere Wolemekezekayo za iyeyu. Nʼchifukwa chake ndabwera naye pamaso pa nonsenu, makamaka kwa inuyo mfumu Agripa, kuti mwina mukamufunsitsa ndikhale ndi choti ndilembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Cifukwa cace ndamturutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.