Acts 25:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atsogoleri anu apite nane pamodzi kumeneko, kuti akamneneze munthuyo ngatidi iye adachitapo cholakwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena mwa atsogoleri anu apite nane kumeneko, kuti akafotokoze mlandu wa munthuyu, ngati anachita kanthu kalikonse kolakwika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.