Acts 25:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Fesito atakhala pakati pao ku Yerusalemu kuja masiku osapitirira asanu ndi atatu kapena khumi, adapita ku Kesareya. M'maŵa mwake adakhala pa mpando woweruzira milandu, naitanitsa Paulo kuti abwere pamaso pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m'mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Festo atakhala nawo masiku asanu ndi atatu kapena khumi iye anapita ku Kaisareya, ndipo mmawa mwake anayitanitsa bwalo nalamula kuti abweretse Paulo pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikiraku Kaisareya; ndipo m'mawa mwace anakhala pa mpando waciweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.