Acts 25:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paulo atafika, Ayuda amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu aja adamzinga, nayamba kumneneza zinthu zoopsa zambiri, zimene iwo sadathe kuzitsimikiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sanakhoza kuzitsimikiza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo atafika, Ayuda amene anafika kuchokera ku Yerusalemu anayima momuzungulira. Iwo anamunenera zinthu zoopsa zambiri zimene sakanatha kubweretsa umboni wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikuru, zimene sanakhoza kuzitsimikiza;