Acts 25:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Fesito pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adafunsa Paulo kuti, “Kodi ungakonde kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakowu ukazengedwere kumeneko pamaso panga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Festo, pofuna kuti Ayuda amukonde anafunsa Paulo kuti, “Kodi iwe ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti kumeneko ukafotokoze mlandu wako pamaso panga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kama Festo pofuna kuyesedwa wacisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?