Acts 26:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidaazichitadi ku Yerusalemu. Akulu a ansembe atandipatsa ulamuliro, ine ndinkaŵatsekera m'ndende anthu ambiri a Mulungu. Pamene iwo ankaphedwa, ine ndinkavomereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chimenenso ndinachita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.