Acts 26:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kaŵirikaŵiri ndinkaŵalanga m'nyumba zonse zamapemphero, ndi kuyesa kuŵakakamiza kuti amnyoze Yesuyo. Ndinkaŵachitira ukali woopsa, kotero kuti ndinkaŵazunza ngakhale ku mizinda ya ku maiko achilendo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumidzi yakunja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.