Acts 26:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa njira, nthaŵi yamasana dzuŵa lili pa mutu, inu amfumu, ndidaona kuŵala kochokera kumwamba. Kuŵalako kunali koposa kuŵala kwa dzuŵa, ndipo kudatizinga tonse, ine ndi anzanga aulendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wolemekezeka Mfumu, nthawi ya masana pamene ndimayenda pa msewu, ndinaona kuwala kuchokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa kutandizungulira ine pamodzi ndi anzangawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kocokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa, kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.