Acts 26:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tonse tidagwa pansi, ndipo ine ndidamva mau ondiwuza pa Chiyuda kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji? Ukungodzipweteka wekha ngati ng'ombe yoponda zidyali pa chobayira.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'cinenedwe ca Cihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? nkukubvuta kutsalima pacothwikira.