Acts 26:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano dzuka ndipo imirira. Ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndiponso mboni ya zimene waziona za Ine ndiponso zimene ndidzakuonetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti cifukwa ca ici ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo we;