Acts 26:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine.