Acts 26:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero. Motero ndaimirira pano kuti ndichite umboni pamaso pa anthu onse, aakulu ndi ang'ono omwe. Zimene ndikuŵauza si zina ai, koma ndi zomwezo zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzachitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero lino. Ine ndayima pano kuti ndichitire umboni kwa anthu onse otchuka ndi anthu wamba. Ine sindikunena zina zowonjezera koma zimene Aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwacitira umboni ang'ono ndi akuru, posanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananenazidzafika;