Acts 26:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paulo adati, “Kaya ndi pa kanthaŵi kochepa kaya nthaŵi yaitali, Mulungu akadalola kuti osati inu nokha, komanso anthu onse amene alikumva mau anga lero, akhale monga momwe ndiliri inemu, kupatula maunyolo okhaŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo anayankha kuti, “Ngakhale kanthawi kochepa kapena nthawi yayitali, ine ndikupempha kwa Mulungu kuti osati inu nokha koma aliyense amene akundimva lero lino akhale monga ine, kupatulapo maunyolo okhawa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndiri ine, osanena nsinga izi.